Nduna ya za maphunziro, sayansi ndi luso lamakono a Bright Msaka yati anthu asadere nkhawa kuti fizi ya msukulu za ukachenjede yakwera.
A Msaka ati izi sizodetsa nkhawa kaamba koti boma laika ndalama zokwanira ku Higher Education Students’ Loans and Grants Board kuti ophunzira atenge, molingana ndi mlingo womwe fiziyi yakwelera.
Iwo anena izi ku m'mawaku pomwe amayankhula ndi akuluakulu pa sukulu ya ukachenjede ya Malawi ku Zomba.
A Msaka ayendera zina mwa zitukuko pa sukulu ya ukachenjedeyi ku Zomba, zomwe wachiwiri kwa mkulu wa sukuluyi, Professor Samson Sajidu wati zithandizira kukwaniritsa masomphenya a dziko lino.
No Comments Yet...