
Mnyamata wazaka 25, Emmanuel Gama, wafa sitima itamuomba pa njanji m'mudzi mwa Sikero, kwa mfumu yaikulu Kalonga m'boma la Salima.
Mneneri wa polisi ya Salima, a Rebecca Ndiwate, watsimikiza za ngoziyi, ponena kuti yachitika masanawa.
A Ndiwate ati pakadali pano apolisi akhazikitsa kafukufuku pofuna kudziwa chomwe chadzetsa ngoziyi.
Malinga ndi malipoti, Gama adalowa mu njanjiyi komanso osasuntha pamene sitimayo imayandikira.
A Emmanuel Gama amachokera m'mudzi wa Chigombe, kwa mfumu yaikulu Kalonga m'boma la Salima.
#Your Voice Your Station
#Kubweretsa Chilungamo Kwa Onse
No Comments Yet...