Mphwawo wa malemu Shanil Dzimbiri, a Argentina Malamulo wauza komiti yakunyumba yamalamulo yomwe ikufufuza ngozi ya ndege kuti pa 10 June, 2024 chakumasana mzawo anawayimbila n'kuwauza ngati aona pamasamba a mchezo kuti azakhali awo anali nawo mu ndege yomwe yasowa.
Iwo ati anayesela kuimbira a Dzimbiri koma sanathe kulumikizana nawo ndipo anapita ku nyumba ya Mayi Dzimbiri komwe anakhala mpaka madzulo akuona nkhaniyi pa masamba amchezo.
Iwo ati mawa lake anthu ena ndi achibale anafika kuti amve zambiri koma sanathe kunena, mpaka mma 10 koloko, pomwe anaona pa masamba amchezo kuti ndege yapezeka ndipo palibe wapulumuka.
A Malamulo ati masana anapita ku Airwing ku Lilongwe komwe aboma anakonza kuti matupi afikile koma anasintha kuti afikila ku bwalo la ndege la Kamuzu.
#KubweretsaChilingamoKwaOnse.
No Comments Yet...